Masalimo 108 - Buku LopatulikaDavide aimbira Mulungu womgonjetsera adani ( Mas. 57.7-11 ; 60.5-12 ) Nyimbo. Salimo la Davide. 1 Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga. 2 Galamukani, chisakasa ndi zeze; ndidzauka ndekha mamawa. 3 Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu. 4 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. 5 Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu; ndi ulemerero wanu pamwamba padziko lonse lapansi, 6 kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze. 7 Mulungu analankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera: ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti. 8 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga; ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga. 9 Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga; ndidzafuulira Filistiya. 10 Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu? 11 Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya osatuluka nao magulu athu? 12 Tithandizeni mumsauko; pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. 13 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi