Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 108:6 - Buku Lopatulika

6 kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tipambanitseni pa nkhondo ndi dzanja lanu lamanja, mundiyankhe kuti ife, okondedwa anu, tipulumuke.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 108:6
22 Mawu Ofanana  

natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.


Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anavomera, nati, Ndiwo mau abwino amene.


Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.


Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.


Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu, ndipo mundiweruze ndi mphamvu yanu.


Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.


Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.


Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.


Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zopambana, zimene suzidziwa.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.


Za Benjamini anati, Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi Iye mokhazikika; am'phimba tsiku lonse, inde akhalitsa pakati pa mapewa ake.


Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa