Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 108:13 - Buku Lopatulika

13 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano, ndipo adzapondereza pansi adani athu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 108:13
13 Mawu Ofanana  

Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.


Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao:


Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo; ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.


Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima, ndipo Iye adzapondereza otisautsa.


Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu uponderezedwa padzala.


Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga; ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zovala zanga; ndipo ndadetsa chofunda changa chonse.


Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.


Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ntchafu, makanthidwe aakulu; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa