Masalimo 98 - Buku LopatulikaAlemekeze Mulungu pa chifundo ndi choonadi chao Salimo. 1 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso. 2 Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake; anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu. 3 Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu. 4 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. 5 Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze; ndi zeze ndi mau a salimo. 6 Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova, ndi mbetete ndi liu la lipenga. 7 Nyanja ifuule ndi kudzala kwake; dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo; 8 mitsinje iombe m'manja; mapiri afuule pamodzi mokondwera. 9 Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi