Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 98:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake; anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake; anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo, waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova waonetsa chipulumutso chake ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 98:2
23 Mawu Ofanana  

Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.


Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.


ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m'Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga.


inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.


Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.


Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.


Ndipo amitundu adzaona chilungamo chako, ndi mafumu onse ulemerero wako; ndipo udzatchedwa dzina latsopano, limene m'kamwa mwa Yehova mudzatchula.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.


ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.


Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.


Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.


Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsate chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;


akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;


Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa