Masalimo 98:4 - Buku Lopatulika4 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi, muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera. Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.