Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.
Masalimo 8:1 - Buku Lopatulika Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi. Kumwamba amaimba nyimbo zotamanda ulemerero wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba. |
Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.
Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.
Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.
Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.
Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?
M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana aakazi inu a ku Yerusalemu.
Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu Ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzatchula dzina lanu.
Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.
Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau.
Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.
Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu;
Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,
Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;
Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.