Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -

Masalimo 8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero


Salimo 8
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.

1 Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba.

2 Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda, Inu mwakhazikitsa mphamvu chifukwa cha adani anu, kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.

3 Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake,

4 munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira, ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?

5 Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.

6 Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu; munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;

7 nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi ndi nyama zakuthengo,

8 mbalame zamlengalenga ndi nsomba zamʼnyanja zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.

9 Inu Yehova, Ambuye athu, dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

The Word of God in Contemporary Chichewa

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®

Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®

Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Biblica, Inc.
Titsatireni:



Zotsatsa