Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
Masalimo 5:8 - Buku Lopatulika Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, ndinu olungama, munditsogolere pakati pa adani ondizonda. Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu chifukwa cha adani anga ndipo wongolani njira yanu pamaso panga. |
Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.
Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere panjira yachidikha, chifukwa cha adani anga.
Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine.
Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
Madzi anandizinga mpaka moyo wanga, madzi akuya anandizungulira, kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.
Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.
ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe.