Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 3:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Paja Yesaya ankanena za iyeyu pamene adaati, “Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Uyu ndi amene mneneri Yesaya ananena za iye kuti, “Mawu a wofuwula mʼchipululu, ‘Konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 3:3
8 Mawu Ofanana  

Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.


Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.


Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa