Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 12:13 - Buku Lopatulika

13 ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:13
15 Mawu Ofanana  

Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.


Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.


Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.


Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale, kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;


Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama, ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;


Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?


Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa