Masalimo 1:6 - Buku Lopatulika Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Chauta amaŵasamalira anthu ake, koma anthu ochimwa adzaonongeka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama, koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka. |
Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse; ndipo mizindayo mwaipasula, chikumbukiro chao pamodzi chatha.
Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.
Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.
Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.
Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.