mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.
Luka 11:4 - Buku Lopatulika Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutikhululukire ife machimo athu, pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mutikhululukire machimo athu, monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ” |
mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.
pamenepo mverani Inu mu Mwambamo, ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.
pamenepo mverani Inu mu Mwamba, ndi kukhululukira tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Aisraele; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula padziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale cholowa chao.
Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.
Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mzinda wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.
Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.
Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.
Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.
Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;
Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?
Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.
Sindipempha kuti muwachotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.
Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.