Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 3:10 - Buku Lopatulika

10 Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza padziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Popeza kuti mwasunga mau anga oti mupirire mosatepatepa, Inenso ndidzakusungani pa nthaŵi yamayeso imene ilikudza m'dziko lonse lapansi, kuti anthu onse okhalamo adzayesedwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Popeza mwasunga mawu anga woti mupirire ndipo mwawugwira mtima, Inenso ndidzakupulumutsani nthawi ya mayesero imene idzabwera pa dziko lonse lapansi kuyesa onse okhala pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 3:10
30 Mawu Ofanana  

Mantha ndi dzenje ndi msampha zili pa iwe, wokhala m'dziko.


Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.


Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.


Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;


Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu.


Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.


Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.


ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:


Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.


Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu:


Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;


Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.


Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.


Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.


Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;


pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.


amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.


Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sangathe kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.


ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?


Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa