Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 13:4 - Buku Lopatulika

4 Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m'Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Nanga anthu aja 18 amene nyumba yosanja idaŵagwera ku Siloamu nkuŵapha? Kodi mukuyesa kuti iwowo anali ophwanya malamulo koposa anthu ena onse okhala m'Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Kapena anthu 18 aja amene anafa nsanja ya Siloamu itawagwera, kodi mukuganiza kuti iwo aja anali ochimwa kwambiri kuposa onse amene amakhala mu Yerusalemu?

Onani mutuwo Koperani




Luka 13:4
13 Mawu Ofanana  

Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mzinda, m'chipinda cha m'katimo.


Ndi Chipata cha ku Kasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pamunda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumzinda wa Davide.


ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.


Popeza anthu awa akana madzi a Siloamu, amene ayenda pang'onopang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya;


Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.


Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu.


Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.


Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.


Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.


Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya.


nati kwa iye, Muka, kasambe m'thamanda la Siloamu (ndilo losandulika, Wotumidwa). Pamenepo anachoka, nasamba, nabwera alikuona.


Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa