Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 2:10 - Buku Lopatulika

10 Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 2:10
36 Mawu Ofanana  

Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.


Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.


Muyesetu anyamata anu masiku khumi; atipatse zomera m'nthaka tidye, ndi madzi timwe.


Ndipo anawamvera mau awa, nawayesa masiku khumi.


Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.


Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.


Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.


Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.


Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.


Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m'dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha.


Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,


Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.


Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.


zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;


Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.


Ndipo chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.


Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwagonjetsa; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.


Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa