Eksodo 4:23 - Buku Lopatulika Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho ndikukuuza kuti umlole mwana wanga apite akandipembedze Ine. Tsono iweyo ukakana, Ine ndidzapha mwana wako wamwamuna wachisamba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ” |
Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.
Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.
ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.
Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.
Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.
Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m'chipululu; koma, taona, sunamvere ndi pano.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.
Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mammawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.