Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 11:1 - Buku Lopatulika

1 Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta akuti, “Pamene Israele anali mwana, ndinkamukonda. Mwana wangayo ndidamuitana kuti atuluke ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Israeli ali mwana, ndinamukonda, ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 11:1
18 Mawu Ofanana  

Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


Inu munaona chimene ndinachitira Aejipito; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.


Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele.


Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.


Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.


Ndachoka kunyumba yanga, ndasiya cholowa changa; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m'dzanja la adani.


Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.


Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukire masiku a ubwana wako, muja unakhala wamaliseche ndi wausiwa, womvimvinizika m'mwazi wako.


Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikuvimvinizika m'mwazi mwako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako. Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.


Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.


Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera mu Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.


Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika.


Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.


Ndipo ndidzampatsa minda yake yampesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.


Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;


nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.


Inde akonda mitundu ya anthu; opatulidwa ake onse ali m'dzanja mwanu; ndipo akhala pansi ku mapazi anu; yense adzalandirako mau anu.


Yehova sanakondwere nanu, ndi kukusankhani chifukwa cha kuchuluka kwanu koposa mitundu ina yonse ya anthu, kapena kuchepera kwanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa