Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 10:15 - Buku Lopatulika

15 Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Momwemo zidzakuchitikirani inu a ku Betele chifukwa cha uchimo wanu waukulu. Nkhondo ikadzangoyamba m'mamaŵa, nayonso mfumu ya ku Israele idzaphedwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu. Tsiku limeneli likadzafika, mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 10:15
8 Mawu Ofanana  

Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Mowabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang'onong'ono ndi achabe.


Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake.


Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?


Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.


Ndipo Samariya, mfumu yake yamwelera ngati thovu pamadzi.


Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.


Ndipo tsopano chabwino chija chinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma uchimo, kuti uoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa ndithu mwa lamulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa