Eksodo 12:29 - Buku Lopatulika29 Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Pakati pa usiku, Chauta adapha ana onse achisamba m'dziko la Ejipito. Adayambira mwana wachisamba wa Farao amene ankayembekezeka kuloŵa ufumu wake, mpaka ana a akaidi a m'nyumba zamdima za m'ndende. Ana onse oyamba kubadwa a nyama adaphedwanso ndithu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo. Onani mutuwo |