Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 8:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Iwowo adachitadi momwemo. Aroni adasamula ndodo yake ija namenya nthaka. Tsono fumbi lonse lidasanduka nthata, ndipo zidabalalikira pa anthu ndi pa nyama zomwe. Motero fumbi lonse la ku Ejipito lidangokhala nthata zokhazokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Iwo anachita momwemo, ndipo pamene Aaroni anakweza ndodo yake ndi kumenya fumbi, nsabwe zinafika pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Fumbi lonse la mʼdziko la Igupto linasanduka nsabwe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:17
7 Mawu Ofanana  

Ananena, ndipo inadza mitambo ya ntchentche, ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse.


Anawatumizira pakati pao mitambo ya ntchentche zakuwatha; ndi achule akuwaononga.


Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.


Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.


Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.


Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa