Eksodo 18:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Ndipo Mose adamufotokozera zonse zimene Chauta adamchita Farao ndi Aejipito chifukwa cha Aisraelewo. Adamsimbiranso za mavuto omwe adaakumana nawo pa njira, ndi zonse zimene Chauta adaachita poŵapulumutsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira. Onani mutuwo |
Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.