Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m'mtima mwake.
Eksodo 32:12 - Buku Lopatulika Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi mukufuna kuti Aejipitowo azidzanena kuti, ‘Adaŵatulutsa ku Ejipito ndi cholinga choipa choti akaŵaphere ku mapiri ndi kuŵaonongeratu pa dziko lapansi?’ Ukali wanu woyaka ngati motowo ubwezeni, ndipo musaŵaononge anthu anu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu. |
Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m'mtima mwake.
pakuti awa ndi anthu anu ndithu, ndi cholowa chanu chimene munatulutsa mu Ejipito, m'kati mwa ng'anjo ya chitsulo;
Ayang'anire ichi tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'mizinda mwathu amene anadzitengera akazi achilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akulu a mzinda wao uliwonse, ndi oweruza ake, mpaka udzatichokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu chifukwa cha mlandu uwu.
Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.
Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.
Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikakamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu.
Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.
Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.
Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.
Koma ndinabweza dzanja langa ndi kuchichita, chifukwa cha dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawatulutsa pamaso pao.
Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito.
Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?
Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.
Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke;
Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Ejipito kufikira tsopano.
Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;
Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.
kuti linganene dziko limene mudatitulutsako, Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa m'dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawatulutsa kuti awaphe m'chipululu.
Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.
Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?
Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.