Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 7:9 - Buku Lopatulika

9 Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Akanani ndi anthu ena onse okhala m'dziko muno adzamva zimenezi, ndipo adzatizinga ndi kutipha tonse. Kodi pamenepa inu mudzachitapo chiyani kuti ulemu wanu usaonongeke?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Akanaani ndi anthu ena a dziko lino adzamva zimenezi ndipo adzatizinga ndi kutiwonongeratu. Nanga inu mudzatani ndi dzina lanu lamphamvulo?”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 7:9
19 Mawu Ofanana  

Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.


Monga dzina lanu, Mulungu, momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi; m'dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.


Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, chifukwa cha dzina lanu.


Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.


Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu.


Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.


Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito.


Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?


Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.


Ndipo Mose anati kwa Yehova, Pamenepo Aejipito adzamva; popeza munakweza anthu awa ndi mphamvu yanu kuwachotsa pakati pao;


Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.


kuti linganene dziko limene mudatitulutsako, Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa m'dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawatulutsa kuti awaphe m'chipululu.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere?


Ndidzanenanji, Ambuye, Israele atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao?


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa