Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 3:9 - Buku Lopatulika

9 Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Nkudziŵanji, mwina Mulungu nkutikhululukira, naleka kutikwiyira, ifeyo osaonongeka.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.”

Onani mutuwo Koperani




Yona 3:9
14 Mawu Ofanana  

Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandichitira chifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.


Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.


Munabweza kuzaza kwanu konse; munabwerera kumkwiyo wanu wotentha.


Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.


Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.


Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.


Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.


Momwemo ananyamula Yona, namponya m'nyanja; ndipo nyanja inaleka kukokoma kwake.


Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike.


Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.


Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.


Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa