Eksodo 14:8 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adaumitsa mtima Farao mfumu ya ku Ejipito, ndipo iye adalondola Aisraele, pamene Aisraele ankachoka monyada. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika. |
Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
Ndipo chizikhala ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chapamphumi pakati pamaso ako; pakuti Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka.
Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
Ndipo Ine, taonani, ndidzalimbitsa mitima ya Aejipito, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yake yonse, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake.
Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.
napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a mu Ejipito, ndi akapitao ao onse.
Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwapeza, ndidzagawa zofunkha; ndidzakhuta nao mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.
Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.
Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka.
Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse,
Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.
ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukulu, ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa;
Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse.
Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.
Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magaleta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako.