Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 13:18 - Buku Lopatulika

18 Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 M'malo mwake Mulungu adaŵadzeretsa njira yozungulira, yachipululu, yopita ku Nyanja Yofiira. Monsemo nkuti Aisraele ali okonzekeratu za nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 13:18
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israele kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kuchokera kuno.


Ndipo anawatsogolera panjira yolunjika, kuti amuke kumzinda wokhalamo.


Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu; pakuti chifundo chake nchosatha.


Dziko lapansi linagwedezeka, inde thambo linakha pamaso pa Mulungu; Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israele.


Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.


Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.


Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.


Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.


Anampeza m'dziko la mabwinja, m'chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m'diso.


Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;


Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;


ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa