Eksodo 13:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Farao ataŵalola Aisraele kuti apite, Mulungu sadaŵadzeretse njira yopita kwa Afilisti, ngakhale kuti imeneyi inali njira yachidule. Mulungu adati, “Sindifuna kuti anthu ameneŵa adzasinthe maganizo ao nadzabwereranso ku Ejipito, akadzangokumana ndi nkhondo yolimbana nawo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.” Onani mutuwo |