Eksodo 14:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Aejipitowo, ndiye kuti akavalo ndi magaleta a Farao, oyendetsa magaletawo, okwera pa akavalo ndi gulu lankhondo la Farao, adalondola Aisraele aja nakaŵapeza pamalo pomwe adaamanga zithando paja, pafupi ndi Pihahiroti, moyang'anana ndi Baala-Zefoni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. Onani mutuwo |