Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 14:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Aejipitowo, ndiye kuti akavalo ndi magaleta a Farao, oyendetsa magaletawo, okwera pa akavalo ndi gulu lankhondo la Farao, adalondola Aisraele aja nakaŵapeza pamalo pomwe adaamanga zithando paja, pafupi ndi Pihahiroti, moyang'anana ndi Baala-Zefoni.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 14:9
5 Mawu Ofanana  

Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo.


“Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni.


Mdaniyo anati, “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira. Ndidzagawa chuma chawo; ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa. Ine ndidzasolola lupanga langa, ndi mkono wanga ndidzawawononga.”


Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli.


Nditatulutsa makolo anu ku Igupto ndinafika nawo ku Nyanja Yofiira. Aigupto anawathamangira ndi magaleta ndi okwera pa akavalo mpaka ku Nyanja Yofiira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa