Levitiko 26:13 - Buku Lopatulika13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo a Aejipito. Ndadula goli lanu kuti muziyenda moongoka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka. Onani mutuwo |