Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 15:9 - Buku Lopatulika

9 Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwapeza, ndidzagawa zofunkha; ndidzakhuta nao mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwapeza, ndidzagawa zofunkha; ndidzakhuta nao mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Mdani uja adati, ‘Ndidzaŵalondola nkuŵagwira. Chuma chao ndidzachigaŵagaŵa, ndipo mtima wanga udzakhutira nacho. Ndidzasolola lupanga, ndipo ndidzaŵaononga ndi dzanja langa.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mdaniyo anati, “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira. Ndidzagawa chuma chawo; ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa. Ine ndidzasolola lupanga langa, ndi mkono wanga ndidzawawononga.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:9
15 Mawu Ofanana  

Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha.


Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga; ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha.


Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.


Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.


Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?


Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.


Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?


Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.


Ndipo anafuula kumeneko, Farao mfumu ya Aejipito ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira.


Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.


koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.


Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.


Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa