Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 15:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mutauzira mpweya wanu, madzi adaunjikana pa malo amodzi. Madzi oyenda adangoima kuti chilili, ngati khoma. Nyanja yozamayo idalimba mpaka pansi pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu madzi anawunjikana pamodzi. Nyanja yakuya ija inasanduka madzi owuma gwaa kufika pansi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:8
13 Mawu Ofanana  

Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.


Atayika ndi mpweya wa Mulungu, nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.


Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu, amakundika zakudya mosungiramo.


Anagawa nyanja nawapititsapo; naimitsa madziwo ngati khoma.


Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka kudziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao.


Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.


Munaponda panyanja ndi akavalo anu, madzi amphamvu anaunjikana mulu.


Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;


Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.


pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa