Eksodo 15:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu madzi anawunjikana pamodzi. Nyanja yakuya ija inasanduka madzi owuma gwaa kufika pansi. Onani mutuwoBuku Lopatulika8 Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Mutauzira mpweya wanu, madzi adaunjikana pa malo amodzi. Madzi oyenda adangoima kuti chilili, ngati khoma. Nyanja yozamayo idalimba mpaka pansi pake. Onani mutuwo |
madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko.