Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 14:7 - Buku Lopatulika

7 napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a mu Ejipito, ndi akapitao ao onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a m'Ejipito, ndi akapitao ao onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Adatenga magaleta amphamvu 600 pamodzi ndi magaleta ena onse ndipo adaika atsogoleri pa magaleta onsewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 14:7
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu.


Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.


Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika.


Ndipo Aejipito anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magaleta ake, ndi apakavalo ake.


Ndipo anamanga galeta lake, napita nao anthu ake;


Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.


Magaleta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m'nyanja; ndi akazembe ake osankhika anamira mu Nyanja Yofiira.


Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magaleta anga ine ndafika kunsonga za mapiri, kumbali za Lebanoni; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pake penipeni, kunkhalango ya munda wake wobalitsa.


Ndipo Yehova anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa