Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 33:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Adanyamuka ku Ramsesi pa mwezi woyamba, pa tsiku la 15 la mweziwo. M'maŵa mwake, litapita tsiku la Paska, Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mokondwa, anthu onse a ku Ejipito akupenya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 33:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m'dziko la Ejipito, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramsesi, monga analamulira Farao.


Ejipito anakondwera pakuchoka iwo; popeza kuopsa kwao kudawagwera.


Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa chaka.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.


Mutuluka lero lino mwezi wa Abibu.


Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.


Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.


Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.


Ndipo Mose analembera matulukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa matulukidwe ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa