Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 14:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chauta adaumitsa mtima Farao mfumu ya ku Ejipito, ndipo iye adalondola Aisraele, pamene Aisraele ankachoka monyada.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 14:8
21 Mawu Ofanana  

Iye anatulutsa anthu ake akukondwera, osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;


Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine; mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo sanafune kuwalola kuti apite.


Ndipo chidzakhala kwa inu ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi pamphumi panu kuonetsa kuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.”


Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo.


Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.


Ine ndidzawumitsa mitima ya Aigupto kotero kuti adzatsatirabe Aisraeli. Ndipo ine ndikadzagonjetsa Farao ndi asilikali ake onse ankhondo, okwera magaleta ndi akavalo, ndidzapeza ulemerero.


Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.


Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo.


Mdaniyo anati, “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira. Ndidzagawa chuma chawo; ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa. Ine ndidzasolola lupanga langa, ndi mkono wanga ndidzawawononga.”


Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite.


Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose.


Phimbani mitima yawo, ndipo matemberero anu akhale pa iwo!


Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.


Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona,


Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu.


Kotero Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndi mkono wotambasuka ndi zoopsa zazikulu ndi zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa.


koma sindinafune kuti adani anga adzandinyoze, mwina adani anga sadzandimvetsetsa ndipo adzanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwa ndife; Yehova sanachite zonsezi.’ ”


Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe.


Ine ndidzakokera Sisera mkulu wa ankhondo a Yabini pamodzi ndi magaleta ake ndi asilikali ake kwa inu ku mtsinje wa Kisoni ndipo ndidzamupereka mʼmanja mwanu.’ ”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa