Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Eksodo 12:51 - Buku Lopatulika Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lomwelo ndi pamene Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito mwa magulumagulu ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.” |
Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.
M'mene Israele anatuluka ku Ejipito, nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo;
Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m'dziko la Ejipito.
Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.
Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito.
Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m'chipululu cha Sinai.
ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao.
Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;
Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu.
kuti mibadwo yanu ikadziwe kuti ndinakhalitsa ana a Israele m'misasa, pamene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.
Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.
Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito.
Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m'dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.
Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.
Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku.
Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito;
Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani.
Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.