Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 12:51 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

51 Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

51 Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

51 Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

51 Pa tsiku lomwelo ndi pamene Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito mwa magulumagulu ao.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:51
25 Mawu Ofanana  

Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.”


Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.


Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Ayuda. Akusi anathawa,


Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,


Natulutsa Israeli pakati pawo, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.


Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto.


“Aisraeli onse anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.


Yehova anati kwa Mose,


Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai.


Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto.


Choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse mʼdzanja la Aigupto, kuwatulutsa mʼdzikolo ndi kukawalowetsa mʼdziko labwino ndi lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi, kwawo kwa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.


Aaroni ndi Mose ndi aja amene Yehova anawawuza kuti, “Tulutsani Aisraeli mu Igupto mʼmagulu awo.”


“Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo.


iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto.


kuti zidzukulu zanu zidzadziwe kuti ndine amene ndinakhazika Aisraeli mʼmisasa nditawatulutsa ku Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”


“Ine ndinakutulutsani ku Igupto, ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kudzakupatsani dziko la Aamori.


Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo. Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni, pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.


Mulungu wowatulutsa mʼdziko la Igupto, ali ndi mphamvu ngati za njati.


“Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:


Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni.


Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu.


Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto.


Popeza anakonda makolo anu ndi kusankha adzukulu awo, a pambuyo pawo, anakutulutsani kuchoka ku Igupto ali pakati panu ndi mphamvu yake,


“ ‘Kenaka ndinatuma Mose ndi Aaroni, ndipo ine ndinazunza Aigupto. Pambuyo pake ndinakutulutsani.


Ngakhale munazidziwa kale zonsezi, ndafuna kuti ndikukumbutseni kuti Ambuye anapulumutsa anthu ake ndi kuwatulutsa mʼdziko la Igupto, koma pambuyo pake anawononga amene sanakhulupirire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa