Masalimo 114 - Buku LopatulikaAlemekeze Mulungu pa chipulumutso chija cha mu Ejipito 1 M'mene Israele anatuluka ku Ejipito, nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo; 2 Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake. 3 Nyanjayo inaona, nithawa; Yordani anabwerera m'mbuyo. 4 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati anaankhosa. 5 Unathawanji nawe, nyanja iwe? Unabwereranji m'mbuyo, Yordani iwe? 6 Munatumphatumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu? Ngati anaankhosa, zitunda inu? 7 Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye, pamaso pa Mulungu wa Yakobo; 8 amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi