Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 114:4 - Buku Lopatulika

4 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati anaankhosa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati anaankhosa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mapiri aakulu adalumphalumpha ngati nkhosa zamphongo, nazonso zitunda zidalumpha ngati anaankhosa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 114:4
14 Mawu Ofanana  

Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.


Aitumphitsa monga mwanawang'ombe; Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.


Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.


Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.


Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje? Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi, kapena ukali wanu panyanja, kuti munayenda pa akavalo anu, pa magaleta anu a chipulumutso?


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa