Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 114:2 - Buku Lopatulika

2 Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Yuda adasanduka malo opatulika a Chauta, Aisraele adasanduka anthu a mu ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 114:2
14 Mawu Ofanana  

Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.


Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao.


ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito.


Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.


popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.


Aimirire awa paphiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.


Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israele wonse, ndi kuti, Khalani chete, imvanitu, Israele; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.


Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa