Masalimo 114 - Mawu a Mulungu mu Chichewa ChaleroSalimo 114 1 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo, 2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake. 3 Nyanja inaona ndi kuthawa, mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo; 4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa. 5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa? iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo? 6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna, inu timapiri, ngati ana ankhosa? 7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi, pamaso pa Mulungu wa Yakobo, 8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime, thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi. |
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Biblica, Inc.