Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 114:1 - Buku Lopatulika

1 M'mene Israele anatuluka ku Ejipito, nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 M'mene Israele anatuluka ku Ejipito, nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pamene Israele adatuluka ku Ejipito, pamene banja la Yakobe lidatuluka kuchokera ku mtundu wa anthu a chilankhulo chachilendo,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 114:1
10 Mawu Ofanana  

Ndipo sanadziwe kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira.


Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.


Ndinamchotsera katundu paphewa pake, manja ake anamasuka ku chotengera.


Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m'dziko la Ejipito.


Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku.


ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukulu, ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa