Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 6:4 - Buku Lopatulika

4 Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Paja Ine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito. Ndidakuwombolani ku dziko laukapololo. Ndipo ndidaachita kutuma Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti akutsogolereni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo. Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni, pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.

Onani mutuwo Koperani




Mika 6:4
29 Mawu Ofanana  

Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?


Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa, ndi dzanja la Mose ndi Aroni.


Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti utulutse anthu anga, ana a Israele mu Ejipito.


Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.


Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.


Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele mu Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.


ndipo munatulutsa anthu anu Israele m'dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;


Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.


Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.


Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m'dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.


Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.


Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.


koma muzikumbukira kuti munali akapolo mu Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi.


Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.


koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya ukapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.


Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawatulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo Samuele ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, natulutsanso makolo anu m'dziko la Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa