Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika.
2 Samueli 15:20 - Buku Lopatulika Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwe wangobwera dzulo. Ndiye ine ndikutenge lero, kuti uzinka nuyenda nane? Ine ndemwe sindikudziŵa kumene ndikupita. Bwerera ndi anthu akwanu, ndipo Chauta akukomere mtima ndi kukuchitira zabwino mwa kukhulupirika kwake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wangobwera dzulo lomweli, lero ndikutenge kuti uziyendayenda ndi ife, pamene ine sindikudziwa kumene ndikupita? Bwerera, ndipo tenga abale ako. Chifundo ndi kukhulupirika zikhale nawe.” |
Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika.
Ndipo tsopano Yehova achitire inu chokoma ndi choonadi; inenso ndidzakubwezerani chokoma ichi, popeza munachita chinthuchi.
Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi, kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake.
Muwerenga kuthawathawa kwanga, sungani misozi yanga m'nsupa yanu; kodi siikhala m'buku mwanu?
Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.
Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.
Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.
Kodi oganizira zoipa sasochera? Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.
Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza.
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.