Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 8:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu azidzangoyenda uku ndi uku kuchoka ku nyanja ina kunka ku nyanja inanso, azidzangoti piringupiringu kuchoka chakumpoto kunka chakuvuma. Azidzafunafuna mau a Chauta, koma osaŵapeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina. Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa, kufunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 8:12
14 Mawu Ofanana  

Pamenepo adzandiitana, koma sindidzavomera; adzandifunatu, osandipeza ai;


Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; koma wozindikira saona vuto m'kuphunzira.


Popanda chivumbulutso anthu amasauka; koma wosunga chilamulo adalitsika.


Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.


Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;


Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.


Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera.


Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.


Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa