Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:13 - Buku Lopatulika

13 Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pamenepo Davide, pamodzi ndi ankhondo ake amene analipo ngati 600, adachokako ku Keila, namayenda chothaŵathaŵa. Saulo atamva kuti Davide wathaŵa ku Keila, adaleka zoŵatuma ankhondo aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Choncho Davide ndi anthu ake, omwe analipo 600, anachoka ku Keila namayenda mothawathawa. Sauli atamva kuti Davide wathawa ku Keila, sanatumizeko ankhondo ake aja.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:13
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.


Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe.


Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera, kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.


Iwo anayang'ana Iye nasanguluka; ndipo pankhope pao sipadzachita manyazi.


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa