Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereke m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereka m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Davide ankabisala m'mapanga m'dziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Monsemo Saulo ankamufunafuna, koma Mulungu sadalole kuti agwidwe ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Davide ankakhala mʼmapanga mʼdziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Sauli ankamufufuza tsiku ndi tsiku, koma Mulungu sanapereke Davide mʼmanja mwake.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:14
19 Mawu Ofanana  

ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,


Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.


Onani, ndikadathawira kutali, ndikadagona m'chipululu.


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.


Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.


Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;


Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta;


Ndipo Davide anaona kuti Saulo adatuluka kudzafuna moyo wake; Davide nakhala m'chipululu cha Zifi m'nkhalango ku Horesi.


Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.


Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.


Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa