Mawu a Mulungu ndi odabwitsa komanso achinsinsi kwambiri m'mbiri ya anthu. Ine ndikuganiza, kodi si chodabwitsa?
M'malemba oyera muli nkhani zambiri zomwe Mulungu amalankhula mwachindunji ndi anthu ake, akuwavumbulira chifuniro chake, akuwapatsa nzeru ndikuwatsogolera m'njira zawo. Kudzera m'mawu Ake, Mlengi amafotokoza chikondi chake chosatha, chilungamo chake, komanso chikhumbo chake chokhala pa ubwenzi ndi ine ndi iwe.
Nthaŵi zina Mulungu amalankhula kudzera mwa aneneri ndi atumiki, akufalitsa mawu ndi ziphunzitso zake. Nthaŵi zina mawu Ake amaonekera m'maloto ndi masomphenya, monga momwe zinalili ndi aneneri a m'Chipangano Chakale. Komanso, Mulungu amalankhulanso kudzera m'chikumbumtima chathu, akutilangiza ndi kunong'oneza m'mitima mwathu pamene tikufunika kuzindikira chifuniro Chake.
Koma Mulungu angalankhulenso kudzera muzomwe zimachitika tsiku ndi tsiku m'miyoyo yathu. Kudzera m'mikhalidwe ndi zochitika zomwe zimawoneka ngati zopanda pake, Mulungu angatilankhule ndikutivumbulira dongosolo lake ndi cholinga chake. Ndikofunikira kukhala tcheru ndi omvera mawu ake, chifukwa angaonekere m'njira zosayembekezereka.
Mawu a Mulungu ndi apadera komanso amphamvu. Mosiyana ndi mawu ena omwe timamva m'dziko lino, mawu a Mulungu satikana, koma amationetsa chikondi chake ndi chifundo chake chosatha. Ndi mawu omwe amatitsogolera m'njira zolungama ndi mtendere, amatilimbikitsa m'nthaŵi zovuta, ndi kutipatsa malangizo pakati pa chisokonezo.
M'Baibulo muli zitsanzo zokhudza mtima za momwe anthu anayankhira mawu a Mulungu. Kuchokera kwa Abrahamu, amene anasiya dziko lake n'kutsatira malangizo a Mulungu kuti akhale tate wa mitundu yambiri, mpaka Mose, amene anatulitsa Aisiraeli mu ukapolo ku Igupto motsogozedwa ndi Mulungu.
Mawu a Mulungu amapitirira malire a nthaŵi ndi malo, akutiitana kuti tidalira Iye ndikumvera malamulo ake. Ine ndikukhulupirira kuti tingathe kumva mawu ake ndikutsata njira zake.
ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.
Liu la Yehova lili pamadzi; Mulungu wa ulemerero agunda, ndiye Yehova pa madzi ambiri.
Liu la Yehova ndi lamphamvu; liu la Yehova ndi lalikulukulu.
Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe; taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.
ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.
Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe pa phiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.
Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.
Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.
umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.
ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.
ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake.
Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto.
Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.
ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m'phiri lopatulika lija.
ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wake, ndi ukulu wake, ndipo tidamva liu lake ali pakati pa moto; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.
amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.
Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.
Ndipo Atate wonditumayo, Iyeyu wandichitira Ine umboni. Simunamva mau ake konse, kapena maonekedwe ake simunaona.
Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.
Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo pa dziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto.
Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zolakika, zimene suzidziwa.
Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova; pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake, ndi okondedwa ake; koma asabwererenso kuchita zopusa.
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.
Mvetsetsani chibumo cha mau ake, ndi kugunda kotuluka m'kamwa mwake.
Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena, kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa?
Ndipo tsopano anthu sakhoza kupenyerera kuunika pakunyezimira kuthambo, ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa.
Kuchokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira, Mulungu ali nao ukulu woopsa.
Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.
M'mwemo anthu amuopa, Iye sasamalira aliyense wanzeru mumtima.
Akumveketsa pansi pa thambo ponse, nang'anipitsa mphezi yake ku malekezero a dziko lapansi.
Mau abuma kuitsata, agunda ndi mau a ukulu wake, ndipo sailetsa atamveka mau ake.
Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ake, achita zazikulu osazidziwa ife.
Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!
Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba, ngati tsiku la ku Masa m'chipululu.
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau akulu, ngati a lipenga,
Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.
Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.
Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.
ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.
Pamene adatulutsa zonse nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mau ake.
Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.
Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona.
Ndipo ambiri anakhulupirira Iye komweko.
Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; chifukwa sizidziwa mau a alendo.
Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.
Pakuti Mulungu alankhula kamodzi, kapena kawiri, koma anthu sasamalira.
M'kulota, m'masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama,
Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.
Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao;
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuka, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi;
Liu la Yehova ligawa malawi a moto.
Liu la Yehova ligwedeza chipululu; Yehova agwedeza chipululu cha Kadesi.
Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi, ndipo lipulula nkhalango; ndipo m'Kachisi mwake zonse zili m'mwemo zimati, Ulemerero.
Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.
Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.
Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.
Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.
Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo, m'kuzisunga izo muli mphotho yaikulu.
Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.
Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.
Palibe chilankhulidwe, palibe mau; liu lao silimveka.
Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,
Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.
Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye.
Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.
Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika chifukwa cha Ine, koma cha inu.
Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akudzindikiritsa ndani?
Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.
Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.
Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.
Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.
Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.
Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.
Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.
Nzeru ifuula panja; imveketsa mau ake pabwalo;
iitana posonkhana anthu polowera pachipata; m'mudzi inena mau ake,
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba.
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:
kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.
Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza; inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.
Aitumphitsa monga mwanawang'ombe; Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati.
Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.
koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.
Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,
Ndipo, Inu, Ambuye, pachiyambipo munaika maziko ake a dziko, ndipo miyamba ili ntchito ya manja anu.
Iyo idzataika; komatu mukhalitsa; ndipo iyo yonse idzasuka monga malaya;
ndi monga chofunda mudzaipinda monga malaya, ndipo idzasanduka; koma Inu ndinu yemweyo, ndipo zaka zanu sizidzatha.
Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala pa dzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?
koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;
Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.
Ndipo Mose anaitana Israele wonse, nanena nao, Tamverani, Israele, malemba ndi maweruzo ndinenawa m'makutu mwanu lero, kuti muwaphunzire, ndi kusamalira kuwachita.
Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.
Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.
Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.
Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!
Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.
Kodi mau anga safanafana ndi moto? Ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?
Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.
Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;
Kodi nzeru siitana, luntha ndi kukweza mau ake?
Landirani mwambo wanga, si siliva ai; ndi nzeru kopambana ndi golide wosankhika.
Pakuti nzeru iposa ngale, ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo.
Ine Nzeru ndikhala m'kuchenjera, ngati m'nyumba yanga; ndimapeza kudziwa ndi zolingalira.
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa; ndine luntha; ndili ndi mphamvu.
Mwa ine mafumu alamulira; akazembe naweruza molungama.
Mwa ine akalonga ayang'anira, ndi akulu, ngakhale oweruza onse a m'dziko.
Akundikonda ndiwakonda; akundifunafuna adzandipeza.
Katundu ndi ulemu zili ndi ine, chuma chosatha ndi chilungamo.
Chipatso changa chiposa golide, ngakhale golide woyengeka; phindu langa liposa siliva wosankhika.
Iima pamwamba pa mtunda, pa mphambano za makwalala;
Ndimayenda m'njira ya chilungamo, pakati pa mayendedwe a chiweruzo,
kuti ndionetse chuma akundikonda, chikhale cholowa chao, ndi kudzaza mosungira mwao.
Yehova anali nane poyamba njira yake, asanalenge zake zakale.
Anandiimika chikhalire chiyambire, dziko lisanalengedwe.
Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine, pamene panalibe akasupe odzala madzi.
Mapiri asanakhazikike, zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa.
Asanalenge dziko, ndi thengo, ngakhale chiyambi cha fumbi la dziko.
Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo; pamene analemba pazozama kwetekwete;
polimbitsa Iye thambo la kumwamba, pokula akasupe a zozama.
Poikira nyanja malire ake, kuti madzi asapitirire pa lamulo lake; polemba maziko a dziko.
pambali pa chipata polowera m'mudzi, polowa anthu pa makomo ifuula:
Ndinali pa mbali pake ngati mmisiri; ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse;
ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu.
Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga.
Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.
Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;
pakuti wondipeza ine apeza moyo; Yehova adzamkomera mtima.
Koma wondichimwira apweteka moyo wake; onse akundida ine akonda imfa.
Ndinu ndikuitanani, amuna, mau anga ndilankhula kwa ana a anthu.
inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
Adzawapereka kumphamvu ya lupanga; iwo adzakhala gawo la ankhandwe.
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.
Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera.
Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.
Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.
Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.
Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga.
Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako.
Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake,
musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu,
Iye sadzafuula, ngakhale kukuwa, pena kumvetsa mau ake m'khwalala.
Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.
Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.
Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba za akaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.
Ndani mwa inu adzatchera khutu lake pamenepo? Amene adzamvera ndi kumva nthawi yakudza?
Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israele, kuti awawanyidwe? Kodi si Yehova? Iye amene tamchimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zake, ngakhale kumvera chiphunzitso chake.
Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m'mtima.
Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera;
ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.
Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.
Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;
Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena?
Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwachita, ndidzakusonyezani amene afanana naye.
Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.
Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa.
Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.
Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?
Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.
Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;
koma chumacho chionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lake mulibe kanthu.
Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake.
Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?
Inde masiku ake onse amadya mumdima, nizimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.
Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.
Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.
Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.
Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.